1 Samuel 21:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo wansembeyo adapereka buledi wachipembedzo kwa Davide, pakuti kunalibe buledi wina, koma buledi yekha woperekedwa kwa Chauta. Buledi wake ndi amene anali atamchotsa pamaso pa Chauta kuti akaikepo wina wamoto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adauchotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anachotsa winawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho wansembe uja anamupatsa buledi wachipembedzo popeza kunalibeko buledi wina aliyense koma yekhayo amene amaperekedwa kwa Yehova. Uyu ndi amene anachotsedwa tsiku limenelo kuti ayikepo wina wotentha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adaucotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anacotsa winawo.