1 Samuel 21:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo munthu wina mwa antchito a Saulo anali pomwepo, pakuti adaayenera kuchita mwambo wachipembedzo ku nyumba ya Chauta. Munthuyo dzina lake anali Doegi Mwedomu, kapitao wa abusa a Saulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsiku limenelo mmodzi wa antchito a Sauli anali pomwepo kudikirira kuti achite mwambo wa chipembedzo mʼnyumba ya Mulungu. Munthuyu dzina lake anali Doegi Mwedomu, munthu wamphamvu pakati pa abusa a Sauli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono munthu wina wa anyamata a Sauli anali komweko, tsiku lija, anacedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lace ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Sauli.