1 Samuel 21:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi kulibe mkondo kuno kapena lupanga? Paja ine sindidabwere ndi lupanga langa kapena zida zanga chifukwa ntchito ya mfumuyo inali yofulumira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? Chifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mlandu wa mfumu ukuti ndifulumire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi muli ndi mkondo kapena lupanga pano? Ine sindinatenge lupanga langa kapena chida china chilichonse chifukwa zimene andituma amfumu ndi zamsangamsanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? cifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mrandu wa mfumu ukuti ndifulumire.