1 Samuel 21:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembeyo adayankha kuti, “Lupanga la Goliyati Mfilisti uja amene mudamupha ku chigwa cha Ela, nlokulunga m'nsalu paseli pa chovala cha efodi. Ngati mufuna, mungathe kutenga limenelo, chifukwa kulibenso lina kuno, koma lokhalo.” Davide adati, “Palibe lina lofanafana ndi limenelo. Patseni lomwelo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembeyo anayankha kuti, “Kuno kuli lupanga la Goliati Mfilisiti uja amene unamupha mʼchigwa cha Ela, lakulungidwa mʼnsalu paseli pa Efodi. Ngati mufuna kulitenga, tengani popeza kuno kulibe lina koma lokhalo.” Davide anati, “Palibe lina lofanana nalo. Ndipatseni lomwelo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati wansembeyo, Lupanga la Goliate Mfilisti munamuphayo m'cigwa ca Ela, onani-liripo lokulunga m'nsaru, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina, Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.