1 Samuel 22:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Saulo adaitanitsa wansembe Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, pamodzi ndi onse a m'banja la bambo wake, amene anali ansembe ku Nobu. Onsewo adabwera kwa mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubi, ndi banja lonse la atate wake, ansembe a ku Nobu; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mfumu inayitanitsa wansembe Ahimeleki mwana wa Ahitubi ndi banja lonse la abambo ake, amene anali ansembe ku Nobi. Ndipo onse anabwera kwa mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubu, ndi banja lonse la atate wace, ansembe a ku Nobi; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu.