1 Samuel 22:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wandichita chiwembu iwe ndi mwana wa Yese? Wampatsa buledi ndi lupanga, ndipo wamfunsira kwa Mulungu zoti achite. Taonani, tsopano wandiwukira, ndipo akundilalira lero lino!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anati kwa iye, Munapangana chiwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Yese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ndi mwana wa Yese mwandiwukira ine? Wamupatsa buledi ndi lupanga. Wafunsiranso kwa Yehova zoti andiwukire ndi kundibisalira monga wachita leromu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anati kwa iye, Munapangana dwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Jese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?