1 Samuel 22:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu zoti achite? Iyai, amfumu! Musandinenere kanthu kena kalikonse koipa, ine mtumiki wanu, kapenanso wina aliyense wa m'banja la bambo wanga, pakuti sindikudziŵa kanthu pa nkhaniyi mpang'ono pomwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi tsiku limeneli linali loyamba kuti ndimufunsire kwa Yehova? Ayi sichoncho! Mfumu musandinenere kanthu kalikonse koyipa kapena banja la abambo anga, pakuti sindikudziwa kanthu kena kalikonse ka zimenezi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wace kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.