1 Samuel 22:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono idauza alonda omwe anali naye kuti, “Apheni ansembe a Chautaŵa, chifukwa akugwirizana ndi Davide. Adaadziŵa kuti Davideyo adathaŵa, koma sadandiwululire zimenezo.” Koma anyamata a mfumuwo sadasamule manja kuti aphe ansembe a Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu niuza asilikali akuima chomzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; chifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululire. Koma anyamata a mfumu sanafune kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mfumu inalamulira alonda amene anali naye kuti, “Iphani ansembe a Yehovawa chifukwa iwo akugwirizana ndi Davide. Iwo amadziwa kuti Davide ankathawa koma sanandiwuze.” Koma antchito a mfumu aja sanasamule dzanja kuti aphe ansembe a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu niuza asilikari akuima comzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; cifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululira. Koma anayamata a mfumu sanafuna kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova.