1 Samuel 22:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo mfumu idauza Doegi kuti, “Kaŵaphe ndiwe.” Doegi, Mwedomu uja, adapitadi kukapha ansembewo. Adapha anthu 85 ololedwa kuvala efodi ya thonje lokoma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akuvala efodi wabafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero mfumu inalamula Doegi kuti, “Uwaphe ndiwe ansembewa.” Choncho Doegi Mwedomu anapita ndi kuwapha. Tsiku limenelo iye anapha amuna 85 amene amavala efodi wa nsalu yofewa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akubvala efodi wabafuta.