1 Samuel 22:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za Nobu, mzinda wa ansembe uja, Saulo adalamula kuti anthu onse okhalamo aphedwe. Choncho amuna ndi akazi, ana ndi makanda, kudzanso ng'ombe, abulu ndi nkhosa, zonsezo adazipha ankhondo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakantha Nobu ndiwo mudzi wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu aamuna ndi aakazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi abulu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena za Nobi, mzinda wa ansembe, Sauli anapha amuna ndi amayi, ana ndi makanda pamodzi ndi ngʼombe, abulu ndi nkhosa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakantha Nobi ndiwo mudzi wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi aburu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.