1 Samuel 22:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwe khala ndi ine, usaope ai, pakuti amene akufuna moyo wako, akufunanso moyo wanga. Ukakhala ndi ine, ukhala pabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ukhale ndi ine, usaopa; popeza iye wakufuna moyo wanga afuna moyo wako; koma ndi ine udzakhala mosungika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe khala ndi ine, usaope munthu amene akufuna moyo wako komanso wanga. Udzatetezeka ukakhala ndi ine.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ukhale ndi ine, usaopa; popeza iye wakufuna moyo wanga afuna moyo wako; koma ndi ine udzakhala mosungika.