1 Samuel 22:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Davide adachoka kumeneko, napita ku Mizipa ku Mowabu. Adapempha mfumu ya ku Mowabu kuti, “Chonde, bwanji bambo wanga ndi mai wanga akhale nao kuno, mpaka nditadziŵa zimene Mulungu adzandichitire.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anachoka kumeneko kunka Mizipa wa ku Mowabu; nati kwa mfumu ya Mowabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga atuluke nakhale nanu, kufikira ndidziwa chimene Mulungu adzandichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kumeneko Davide anapita ku Mizipa ku Mowabu ndipo anapempha mfumu ya Mowabu kuti, “Bwanji abambo ndi amayi anga akhale nanu mpaka ine nditadziwa chimene Mulungu adzachite nane?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anacoka kumeneko kunka ku Mizipa wa ku Moabu; nati kwa mfumu ya Moabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga aturuke nakhale nanu, kufikira ndidziwa cimene Mulungu adzandidtira.