1 Samuel 22:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mneneri Gadi adauza Davide kuti, “Musakhale pano. Muchoke, mupite ku dziko la Yuda.” Pomwepo Davide adachoka, nakaloŵa m'nkhalango ya Hereti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; chokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anachokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mneneri Gadi anawuza Davide kuti, “Usakhale ku phanga kuno. Pita ku dziko la Yuda.” Kotero Davide anachoka ndi kupita ku nkhalango ya Hereti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; cokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anacokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.