1 Samuel 22:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Saulo adamva kuti Davide ndi anthu ake adapezeka. Tsiku limenelo Sauloyo adaakhala pansi patsinde pa mtengo wa mbwemba womera pa chitunda china ku Gibea, mkondo uli m'manja, ankhondo ake atamzungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakumva Saulo kuti anadziwika Davide, ndi anthu ake akukhala naye, Saulo analikukhala m'Gibea, patsinde pa mtengo wa bwemba, m'dzanja lake munali mkondo wake, ndi anyamata ake onse anaimirira pali iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anamva kuti Davide ndi anthu ake apezeka. Nthawiyo nʼkuti Sauli atakhala pansi pa mtengo wa bwemba pa phiri la ku Gibeya, mkondo uli mʼdzanja lake ndi ankhondo ake atayima chomuzungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakumva Sauli kuti anadziwika Davide, ndi anthu ace akukhala naye, Sauti analikukhala m'Gibeya, patsinde pa mtengo wa kumsanje, m'dzanja lace munali mkondo wace, ndi anyamata ace onse anaimirira pali iye.