1 Samuel 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye Sauloyo adafunsa ankhondo ake aja kuti, “Imvani tsono inu Abenjamini. Kodi mwana wa Yese adzakupatsani minda aliyense mwa inu? Kodi adzakusandutsani atsogoleri a magulu ankhondo nonsenu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yamphesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anafunsa ankhondo ake aja kuti, “Tamverani inu anthu a fuko la Benjamini! Kodi mwana wa Yese adzakupatsani nonsenu minda ndi minda ya mpesa? Kodi nonsenu adzakuyikani kukhala atsogoleri a magulu ankhondo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anati kwa anyamata ace akuima comzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Jese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yamphesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;