1 Samuel 22:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina nchifukwa chaketu mukundichita chiwembu chotere. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adandiwululira pamene mwana wanga ankagwirizana ndi mwana wa Yese. Palibe ndi mmodzi yemwe amene akulabadako za ine kapena kundinong'onezako kuti mwana wanga wautsa mtima wa munthu wanga Davide kuti andiwukire, monga akuchitira leromu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwinatu nʼchifukwa chake mwagwirizana zondichita chiwembu. Palibe amene anandiwuza pamene mwana wanga ankapanga pangano ndi mwana wa Yese. Palibe aliyense amene ankalabadirako za ine kapena kundiwuza kuti mwana wanga wautsa mtima wa wantchito wanga kuti andiwukire monga wachitira lero.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti inu nonse munapangana dwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Jese, ndipo palibe wilia wa inu wakundidtira cifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe?