1 Samuel 23:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adalankhula ndi Mulungu kuti, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndithudi, ine mtumiki wanu ndamva kuti Saulo akufunafuna kubwera kuno ku Keila, kuti adzaononge mzindawu chifukwa cha ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, mnyamata wanu wamva zoona kuti Saulo afuna kudza ku Keila, kuononga mudziwo chifukwa cha ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide anayankhula ndi Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, ine mtumiki wanu ndamva ndithu kuti Sauli akufuna kubwera ku Keila ndi kudzawononga mzindawu chifukwa cha ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israyeli, mnyamata wanu wamva zoona kuti Sauli afuna kudza ku Keila, kuononga mudziwo cifukwa ca ine.