1 Samuel 23:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi anthu a ku Keila adzandipereka kwa Saulo? Kodi Saulo adzabweradi monga m'mene ine mtumiki wanu ndamvera? Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndikukupemphani kuti mundiwuze, ine mtumiki wanu.” Chauta adati, “Saulo abweradi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m'dzanja lake? Kodi Saulo adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israele, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi anthu a Keila adzandipereka mʼmanja mwa Sauli? Kodi Sauli abweradi monga ndamvera ine mtumiki wanu? Inu Yehova Mulungu wa Israeli, chonde, ndiwuzeni ine mtumiki wanu.” Ndipo Yehova anati, “Sauli abweradi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m'dzanja lace? Kodi Sauli adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israyeli, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika.