1 Samuel 23:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adafunsanso kuti, “Kodi anthu a ku Keila adzandipereka ine ndi anthu anga kwa Saulo?” Chauta adati, “Inde adzakupereka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafunsanso, “Kodi anthu a ku Keila adzapereka ine ndi anthu angawa kwa Sauli?” Ndipo Yehova anayankha, “Iwo adzakuperekanidi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Sauli? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.