1 Samuel 23:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Davide, pamodzi ndi ankhondo ake amene analipo ngati 600, adachokako ku Keila, namayenda chothaŵathaŵa. Saulo atamva kuti Davide wathaŵa ku Keila, adaleka zoŵatuma ankhondo aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero Davide ndi anyamata ake, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, natuluka ku Keila, nayendayenda kulikonse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Saulo kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide ndi anthu ake, omwe analipo 600, anachoka ku Keila namayenda mothawathawa. Sauli atamva kuti Davide wathawa ku Keila, sanatumizeko ankhondo ake aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero Davide ndi anyamata ace, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, naturuka ku Keila, nayendayenda kuli konse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Sauli kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.