1 Samuel 23:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu a ku Zifi adapita kwa Saulo ku Gibea, nakamuuza kuti, “Davide akubisala ku dera lakwathu m'mapanga a ku Horesi pa phiri la Hakila limene lili kumwera kwa Yesimoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya ndipo anamuwuza kuti, “Davide akubisala kwathu, mʼmapanga a ku Horesi, mʼphiri la Hakila, kummwera kwa Yesimoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Sauli ku Gibeya, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango, m'phiri la Hakila. Umene Uri kumwera kwa cipululu?