1 Samuel 23:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adabwerera ku Zifi, Saulo asananyamuke. Pa nthaŵiyo Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni ku Araba, kumwera kwa Yesimoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Saulo; koma Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, m'chigwa cha kumwera kwa chipululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero iwo ananyamuka ndi kupita ku Zifi, koma Sauli asananyamuke. Nthawi imeneyi Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, ku Araba kummwera kwa Yesimoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Sauli; koma Davide ndi anthu ace anali ku cipululu ca Maoni, m'cigwa ca kumwera kwa cipululu.