1 Samuel 23:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Saulo ndi anthu ake adapita kukamfunafuna Davide, koma iye anali atazimva. Nchifukwa chake adathaŵa napita ku thanthwe la ku chipululu cha Maoni. Saulo atamva kuti Davide adathaŵira ku Maoni, adamlondola kuchipululu komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo ndi anthu ake anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; chifukwa chake anatsikira kuthanthweko, nakhala m'chipululu cha Maoni. Ndipo pamene Saulo anamva ichi, iye anamlondola Davide m'chipululu cha Maoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli ndi anthu ake anapita kukamufufuza Davide. Koma Davide atamva izi anathawa ndi kukabisala ku thanthwe la chipululu cha Maoni. Sauli atamva kuti Davide anathawira ku Maoni anamutsatira ku chipululu komweko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli ndi anthu ace anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; cifukwa cace anatsikira kuthanthweko, nakhala m'cipululu ca Maoni. Ndipo pamene Sauli anamva ici, iye anamlondola Davide m'cipululu ca Maoni.