1 Samuel 23:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adadzera mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake adadzeranso mbali ina ya phirilo. Tsono Davide ndi anthu ake adafulumira kuthaŵa, pamene Saulo ndi anthu ake anali pafupi kuŵagwira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anamuka mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake kuseri kwake; ndipo Davide anafulumira kuthawa, chifukwa cha kuopa Saulo; popeza Saulo ndi anthu ake anazinga Davide ndi anthu ake kwete kuti awagwire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli amayenda mbali ina ya phirilo, ndipo Davide ndi anthu ake nawonso anali mbali ina ya phirilo. Koma Davide ndi anthu ake anafulumira kumuthawa Sauli pamene Sauliyo ndi anthu ake ali pafupi kuwagwira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anamuka mbali yina ya phiri, Davide ndi anthu ace kutseri kwace; ndipo Davide anafulumira kuthawa, cifukwa ca kuopa Sauli; popeza Sauli ndi anthu ace anazinga Davide ndi anthu ace kwete kuti awagwire.