1 Samuel 23:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Saulo adalekeza kulondola Davide, napita kukamenyana ndi Afilisti. Nchifukwa chake malo amenewo adaŵatchula Mwala wa malekano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Saulo anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; chifukwa chake anatchula dzina lake la malo aja, Thanthwe lolekanitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Sauli analeka kuthamangitsa Davide ndipo anapita kukamenyana ndi Afilisti. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Mwala wa Malekano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Sauli anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; cifukwa cace anachula dzina lace la malo aja, Thanthwe lolekanitsa.