1 Samuel 23:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Davide anthu ake adamuuza kuti, “Ngati tikuchita mantha ku Yuda konkuno, nanga nanji tikapita ku Keila kuti tikamenyane ndi magulu ankhondo a Afilisti? Kodi sitikaopa kwambiri kumeneko?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Taonani, ife tikhalira m'mantha ku Yuda kuno; koposa kotani nanga tikafika ku Keila kuponyana ndi makamu a nkhondo a Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu amene anali ndi Davide anati, “Ngati tikuchita mantha ku Yuda konkuno, nanji kupita ku Keila kukamenyana ndi ankhondo a Afilisti!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Taonani, ife tikhalira m'mantha ku Yuda kuno; koposa kotani nanga tikafika ku Keila kuponyana ndi makamu a nkhondo a Afilisti.