1 Samuel 23:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide ndi anthu ake aja adapita ku Keila, ndipo adakamenyana nawo Afilistiwo. Adapha ankhondo ambiri nalanda ng'ombe zao. Choncho Davide adapulumutsa anthu amene ankakhala ku Keila.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala m'Keila.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Keila kukamenyana ndi Afilisti. Anapha Afilisti ambiri ndi kutenga ziweto zawo. Choncho anapulumutsa anthu a ku Keila.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Davide ndi anthu ace anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri Motero Davide analanditsa okhala m'Keila.