1 Samuel 23:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Abiyatara, mwana wa Ahimeleki, adathaŵira kwa Davide ku Keila, adabwera atatenga efodi yaunsembe ija m'manja mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Pamene Abiatara mwana wa Ahimeleki anathawira kwa Davide anabwera ndi efodi mʼmanja mwake).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali kuti Abyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lace.