1 Samuel 23:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo atamva kuti Davide wafika ku Keila, adati, “Mulungu wampereka m'manja mwanga. Pamene waloŵa mu mzinda umene uli ndi zipata ndi mipiringidzo yolimba, ndiye kuti wadzimanga yekha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli atamva kuti Davide wapita ku Keila anati, “Mulungu wamupereka kwa ine, pakuti Davide wadzitsekera yekha mʼndende polowa mu mzinda umene uli ndi zipata ndi zotsekera zake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anauza Sauli kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Sauli anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.