1 Samuel 24:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lero mwaonatu ndi maso anu kuti Chauta anakuperekani m'manja mwanga m'phanga muja. Ena ankandikakamiza kuti ndikupheni, koma ndakulekani dala. Ndinati, ‘Sindipweteka mbuyanga, poti ngwodzozedwa wa Chauta.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lero lino inu mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga mʼphanga muja. Ena anandiwuza kuti ndikupheni, koma ndakusiyani. Ndinati, ‘Sindidzapha mbuye wanga pakuti ndiye wodzozedwa wa Yehova.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, Sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; cifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.