1 Samuel 24:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atate anga, onanitu chidutswa cha mkanjo wanu chili m'manja mwangachi. Pamenepo mudziŵe kuti mumtima mwanga mulibe cholakwa kapena zokuukirani, poti ndadula chidutswa ku mkanjo wanu, koma osakuphani. Sindidakulakwireni, ngakhale kuti inuyo mukufunafuna moyo wanga kuti mundiphe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe coipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakucimwirani, cinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire,