1 Samuel 24:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atamaliza kulankhula mau ameneŵa, Saulo adafunsa kuti, “Kani liwu limeneli ndi lakodi, mwana wanga Davide?” Apo Saulo adayamba kulira mokweza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Saulo, Saulo anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Saulo nakweza mau ake, nalira misozi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Sauli, Sauli anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Sauli nakweza mau ace, nalira misozi.