1 Samuel 24:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Undilonjeze molumbira tsono m'dzina la Chauta kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira, kuti dzina langa ndi la abambo anga lisaiŵalike.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano undilonjeze molumbira lero mʼdzina la Yehova kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira kapena kufuta dzina langa pa banja la makolo anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga.