1 Samuel 24:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adafika ku makola a nkhosa a pamphepete pa njira, pamene panali phanga. Saulo adaloŵa m'phangamo kuti akadzithandize. Pamenepo nkuti Davide ndi anthu ake akubisala m'kati mwenimweni mwa phangalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Sauli analowa kuti akapfunde mapazi ace. Ndipo Davide ndi anyamata ace analikukhala m'kati mwa phangamo,