1 Samuel 24:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthu a Davide aja adamuuza kuti, “Tsiku lija ndi lero limene Chauta ankanena, muja adaakuuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wako m'manja mwako, udzamchita zomwe zidzakukomere.’ ” Tsono Davide adanyamuka, nakadulako chidutswa ku mkanjo wa Saulo, iyeyo osadziŵako ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anthu a Davide anamuwuza kuti, “Tsiku lija lafika limene Yehova anakuwuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wanu mʼmanja mwanu, ndi kumuchita chimene chidzakukomereni.’ ” Koma Davide anapita mwakachetechete ndi kukadula msonga ya mkanjo wa Sauli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamcitira iye cokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli mobisika.