1 Samuel 24:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Davide atalankhula mau ameneŵa, anthu ake adamvera, pakuti sadaŵalole kuti amthire nkhondo Saulo. Pamenepo Saulo adatuluka m'phanga muja namapita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Davide analetsa anyamata ake ndi mau awa, osawaloleza kuukira Saulo. Ndipo Saulo ananyamuka, natuluka m'phangamo, namuka njira yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Davide analetsa anyamata ace ndi mau awa, osawaloleza kuukira Sauli. Ndipo Sauli ananyamuka, naturuka m'phangamo, namuka njira yace.