1 Samuel 25:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Davide adauza ankhondo ake kuti, “Munthu aliyense amangirire lupanga lake.” Choncho aliyense adamangirira lupanga lake. Davide nayenso adamangirira lake. Anthu amene adapita ndi Davide analipo ngati 400. Koma anthu 200 adatsalira kuti azisunga katundu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anawuza anthu ake kuti, “Aliyense amangirire lupanga lake!” Choncho aliyense anamangirira lupanga lake. Davidenso anamangirira lupanga lake. Anthu pafupifupi 400 ndiwo anapita ndi Davide, pamene anthu 200 anatsala ndi katundu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati kwa anthu ace, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lace. Namangirira munthu yense lupanga lace; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lace; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.