1 Samuel 25:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wanchito wina adauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, “Davide adatuma amithenga kuchokera ku chipululu kuti adzalonjere mbuyathu, koma iwo adaŵakalipira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mnyamata wina anauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akuchokera kuchipululu kulonjera mbuye wathu; koma iye anawakalipira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mmodzi mwa antchito anawuza Abigayeli mkazi wa Nabala kuti, “Davide anatumiza amithenga kuchokera ku chipululu kudzalonjera mbuye wathu, koma iye anawalalatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mnyamata wina anauza Abigayeli, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akucokera kucipululu kulankhula mbuye wathu; koma iye anawakalipira.