1 Samuel 25:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndati mudziŵe zimenezi, ndipo muganizirepo zoti muchite, pakuti zimenezi zidzaonongetsa mbuyathu pamodzi ndi banja lao lonse. Chinanso nchakuti mbuyathu aja ndi a khalidwe lovuta, kotero kuti wina aliyense sangathe kulankhula nawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono onani chimene mungachite, chifukwa zimenezi zingadzetse tsoka pa mbuye wathu pamodzi ndi nyumba yake. Paja mbuye athu aja ndi munthu wa khalidwe loyipa moti palibe amene angathe kuyankhula naye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono mudziwe ndi kulingalira cimene mudzacita; popeza anatsimikiza mtima kucitira coipa mbuye wathu, ndi nyumba yace yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.