1 Samuel 25:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mwamsanga Abigaile adatenga mitanda yabuledi 200, matumba achikopa aŵiri a vinyo, nkhosa zisanu zootcheratu, makilogramu 17 a tirigu wokazinga, nchinchi za mphesa zoumika 100, ndiponso makeke ankhuyu 200. Zonsezo adazisenzetsa abulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Abigaile anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoochaocha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri, naziika pa abulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Abigayeli sanataye nthawi. Iye anatenga malofu a buledi 200, matumba a chikopa awiri a vinyo, nkhosa zisanu zowotcheratu, makilogalamu 17 a tirigu wokazinga, makeke a mphesa zowuma 100, ndiponso makeke a nkhuyu 200, ndipo anazisenzetsa abulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Abigayeli anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoocaoca, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi ncinci za mphesa zouma zana limodzi, ndi ncinci za nkhuyu mazana awiri, naziika pa aburu.