1 Samuel 25:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono panali munthu wina ku Maoni amene anali ndi kadziko ku dera la mudzi wa Karimele. Munthuyo anali wolemera kwambiri. Anali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Tsiku lina adayamba kumeta nkhosa zake ku Karimele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wake anali ku Karimele; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi chikwi chimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zake ku Karimele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunali munthu wina wolemera kwambiri ku Maoni amene malo ake a ntchito anali ku Karimeli. Iyeyu anali ndi mbuzi 1,000 ndi nkhosa 3,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wace anali ku Karimeli; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi cikwi cimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zace ku Karimeli.