1 Samuel 25:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵiyo nkuti Davide atanena kuti, “Ndithudi ndidavutika pachabe kutchinjiriza zinthu zonse za munthu ameneyu, zimene anali nazo ku chipululu, kotero kuti palibe kanthu nkamodzi komwe pa zinthu zakezo kamene kadasoŵa. Koma iye wandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m'chipululu, sikadasowa kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawiyi nʼkuti Davide atanena kuti, “Kani ndinalondera pachabe katundu wa munthu uyu mʼchipululu muja! Ndipotu palibe kanthu nʼkamodzi komwe kake kamene kanasowa. Tsono wandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga cabe zace zonse za kaja kanali nazo m'cipululu, sikadasowa kanthu ka zace zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.