1 Samuel 25:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mbuyanga, ndi Chauta yemwe amene wakuletsani kuti musaphe munthu ndi kulipsira ndi manja anu. Inu muli apa, pali Chauta wamoyo, ndikulonjeza molumbira kuti onse amene afuna kukuchitani choipa, adzalangidwa ngati Nabala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mbuye wanga muli apa, ndikulumbira pali Yehova wamoyo amene wakuletsani kuti musakhetse magazi a munthu ndi kulipsira nokha, kuti adani anu amene afuna kukuchitani zoyipa adzakhale ngati Nabala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera cilango ndi dzanja la inu nokha, cifukwa cace adani anu, ndi iwo akufuna kucitira mbuye wanga coipa, akhale ngati Nabala.