1 Samuel 25:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chonde, mukhululukire cholakwa cha ine mdzakazi wanu. Zoonadi, Chauta adzakhazikitsa banja lanu mu ufumu, poti mukummenyera nkhondo. Motero choipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chonde khululukani zolakwa za ine mdzakazi wanu. Ndithu Yehova adzakhazikitsa banja la mbuye wanga mu ufumu, popeza mukumenya nkhondo ya Yehova. Choncho choyipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka coipa masiku anu onse.