1 Samuel 25:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo anali Nabala, wa fuko la Kalebe, ndipo mkazi wake anali Abigaile. Mkaziyo anali wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wakeyo anali wouma mtima ndi wankhanza. Anali wa fuko la Kalebe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzina lake linali Nabala ndipo anali wa fuko la Kalebe. Dzina la mkazi wake linali Abigayeli. Anali mkazi wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wake, wa banja la Kalebe, anali wowuma mtima ndi wamwano pa zochita zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wace ndiye Abigayeli; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa macitidwe ace; ndipo iye anali wa banja la Kalebi.