1 Samuel 25:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo inu simudzamva chisoni kapena kuvutika mu mtima kuti mudakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Ndipo pamene Chauta adzakuchitirani zabwino zonsezi, musadzandiiŵale ine mdzakazi wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mudzakhala opanda chakudodoma nacho, kapena chakusauka nacho mtima wa mbuye wanga, chakuti munakhetsa mwazi wopanda chifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera chilango ndipo Yehova akadzachitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukire mdzakazi wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zikadzatero, inu mbuye wanga simudzakhala ndi chikumbumtima choti munakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Koma Yehova akadzakuchitirani zabwino zonsezi musadzandiyiwale ine mdzakazi wanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mudzakhala opanda cakudodoma naco, kapena cakusauka naco mtima wa mbuye wanga, cakuti munakhetsa mwazi wopanda cifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera cilango; ndipo Yehova akadzacitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukile mdzakazi wanu.