1 Samuel 25:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wa Israele, ndiye wandiletsa kuti ndisakupwetekeni. Zoonadi, pali Chauta, Mulungu wamoyo, mukadapanda kudzakumana nane msanga, ndithu sipakadamtsalira Nabala munthu wamwamuna ndi mmodzi yemwe maŵa m'maŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena zoona, pali Yehova Wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene wandiletsa kuti ndisakupwetekeni, mukanapanda kubwera msanga kudzakumana nane, palibe munthu aliyense wamwamuna wa Nabala akanasiyidwa wamoyo pakucha mmawa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundicingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutaca kanthu konse, ngakhale mwana wamwamunammodzi.