1 Samuel 25:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abigaile adabwerera kwa Nabala nampeza m'nyumba mwake akuchita phwando lalikulu ngati la mfumu. Nabala anali wosangalala mumtima mwakwe, poti anali ataledzera kwambiri. Tsono mkazi wakeyo sadamuuze kanthu kalikonse mpaka m'maŵa kutacha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuza kanthu konse, kufikira kutacha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abigayeli atabwerera kwa Nabala anamupeza ali mʼnyumba akuchita mphwando ngati la mfumu. Iye anali atakondwa kwambiri popeza anali ataledzera kwambiri. Choncho mkazi wakeyo sanamuwuze kalikonse mpaka mmawa kutacha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abigayeli anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwace, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwace, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuza kanthu konse, kufikira kutaca.