1 Samuel 25:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake, m'maso mwa Nabala mutayera, mkazi wakeyo adamuuza zonse. Pomwepo Nabala mtima wake udaima, ndipo thupi lidangoti gwa ngati mwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono m'mawa vinyo atamchokera Nabala, mkazi wake anamuuza zimenezi; ndipo mtima wake unamyuka m'kati mwake, iye nasanduka ngati mwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mmawa, mowa utamuchoka Nabala, mkazi wake anamuwuza zonse. Pomwepo mtima wake unaleka kugunda ndipo unawuma gwaa ngati mwala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono m'mawa vinyo atamcokera Nabala, mkazi wace anamuuza zimenezi; ndipo mtima wace unamyuka m'kati mwace, iye nasanduka ngati mwala.