1 Samuel 25:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide atamva kuti Nabala wafa, adati, “Atamandike Chauta amene walipsira chipongwe chimene adandichita Nabala, ndipo wandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choipa. Chauta wabwezera pamutu pa Nabala ntchito zake zoipa.” Tsono Davide adatuma anyamata ake kukafunsira mbeta Abigaile kuti akhale mkazi wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Davide anamva kuti Nabala wamwalira, iye anati, “Alemekezeke Yehova, walipsira Nabala chipongwe chimene anandichita ndipo anandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choyipa. Yehova wabwezera pamutu pa Nabala choyipa chimene iye anachita.” Kenaka Davide anatumiza mawu kwa Abigayeli, kumupempha kuti akhale mkazi wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mrandu wa mtonzo wanga wocokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wace pa coipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala coipa cace. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigayeli, zakuti amtengere akhale mkazi wace.